Sabata yatha ndinali pa maliro ena ake kwa Kauma, mpepete mwa New State House ku Lilongwe nde ndinatolapo zinthu zingapo zokamba anthu. Zina zoseketsa, zina zomvetsa chisoni
Maphwando ku Kanengo
Panali mdala wina wake amene wadya pension yake mu Spetember 2007. Ndinawayandikira nde amafotokozera anthu ena zama party amene ankachitika ku company kumene ankagwirako. Akuti ku company-ko akagulitsa makina yoposera K1million kunkalizidwa belo, ndekuti anthu onse adziwe kuti kuli kudya ndi kumwa. Mabwana amakagula mowa wokwana 60 litres ndi zakudya zosiyanasiyana ku Hungry Lion takeaway. Ndekuti kumakhala kudyerera usiku wonse mpakana pamene ankatoperapo. Zikatero mmawa anthu amabweretseratu mabotolo akale a Sobo a 2 litres kuti madzulo atungiremo mowa wotsalawo. Komatu masana onse anthu akugwira ntchito akuti amapita kumakatunganso pang’ono namwa mpakana tsiku kutha. Chimene chinandidabwitsa nkuti company imeneyi imagulitsa ma katapila (earth moving equipment) ndiyeno ngati phwando limachitika pakagulitsidwa katundu wa K1million ndekuti maphwando nde amachitika.
Akuba kusowetsa mtendere
Kwa Kauma ko akuba akusowetsa anthu mtendere osati masewera. Nde ena anzeru zawo zolosera akuti ku Mozambique kunayambanso choncho kuti nkhondo yapachiweniweni iyambike. Akuba ankaba mmanyumba mpakana katundu wa anthu anatha. Kenako anayamba kumaba mmagrocery. Katunda amaneyo atamaliza kuba anayamba kumaphana nkutibulana basi kenako nkhondo yapachiweniweni inayambika. Nde poti ndi ma neighbours a state house basi akuwona kuti nkhondo yayambika ndithu.
Mayi alira mwana wake
Tilikudikira ku mortuary ku central, mu chipatala munatuluka anamwino ndi trolley pali mtembo wa mwana, mbuyomo muli amayi olira kuperekeza malirowo. Malirowo atayikidwa mmortuary, azimayi aja anabwera kudzakhala pa kapinga pafupi nafe namafotokoza zimene zinawachitikira. Zimawoneka kuti anthu anabwera ndi mwana wodwalika ndithu koma azachipatala analephera kuwathandiza mpakana mwanayo kuwasiya. Akuti akaphempha kuti mwanayo awonedwe, amakalipiridwa kuti “Ndili ndi manja angati kodi ine? Ndiyankheni, ndilindi manja angati”. Azimayi aja kulephera kunena kuti alipo awiri inde koma tawonani mwanayu chibwerereni sanathandizidwe, koma amapitiriza kufunsa kuti manja alinawo angati. Masiku nkutha mpakana mwana kumwalira.
Ndikhulupirira kuti Chichewachi chinali chochakuka bwino! Pepani ngati muli mwina molakwika pokuti Chinyanja Spell Checker is still under development!!
No comments:
Post a Comment